Isaiah 5:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzapereka chizindikiro kuitana mtundu wa anthu akutali. Adzaŵaitana anthuwo ndi khweru, kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Tsono iwo adzabweradi mothamanga kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutali mbendera, nadzawaimbira mluzu, achokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msangamsanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali, akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Awo akubwera, akubweradi mofulumira kwambiri!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutari mbendera, nadzawayimbira mluzu, acokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msanga msanga;