Isaiah 5:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mivi yao ndi yakuthwa, mauta ao onse ngokoka, ziboda za akavalo ao nzolimba ngati mwala, magaleta ao ndi aliŵiro ngati kamvulumvulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene mivi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kamvulumvulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mivi yawo ndi yakuthwa, mauta awo onse ndi okoka, ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi, magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene mibvi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kabvumvulu;