Isaiah 5:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kufuula kwao kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango, imene imadzuma pogwira nyama, nipita nazo popanda ndi mmodzi yemwe wozipulumutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango; imadzuma pamene ikugwira nyama ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kubangula kwao kudzafana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naicotsa bwino opanda wakupulumutsa.