Isaiah 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye wokondedwa wanga akuti, “Inu amene mumakhala ku Yerusalemu, ndi inu anthu a ku Yuda, ndakupembani, taweruzani pakati pa ine ndi munda wanga wamphesawu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, inu okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wamphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda, weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, inu okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wamphesa.