Isaiah 5:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo adzaŵakokolola monga momwe mtsinje waukulu umakokololera chilichonse chomwe chili mu njira yake ndi mkokomo wa madzi amphamvu. Ndipo wina kuti ayang'ane dzikolo, adzangoona mdima ndi zovuta. Ngakhale kuŵala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja. Ndipo wina akakayangʼana dzikolo adzangoona mdima ndi zovuta; ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yace.