Isaiah 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi chilipo chinanso chimene ndidaayenera kuuchitira munda wanga wamphesa, koma sindidachite? Pamene ndinkayembekeza kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji udabala mphesa zachabechabe?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa kupambana chomwe ndawuchitira kale? Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji unabala mphesa zosadya?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikanacitanso ciani ndi munda wanga wamphesa, cimene sindinacite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?