Isaiah 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsonotu munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonseyo ndi dziko la Israele, ndipo Ayuda ndiwo mipesa yake yokondweretsa. Iye ankayembekeza ntchito zabwino, koma adangoona kuphana. Ankayembekeza chilungamo, koma adangomva kulira kwa anthu ozunzidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti munda wamphesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse ndi Aisraeli, ndipo anthu a ku Yuda ndiwo minda yake yomukondweretsa. Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana; mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti munda wamphesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israyeli, ndi anthu a Yuda, mtengo wace womkondweretsa; Iye anayembekeza ciweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza cilungamo, koma onani kupfuula.