Isaiah 50:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Ili kuti kalata yake imene ndidasudzulira mai wanu? Mwa anthu amene ndili nawo ndi ngongole, ndidakugulitsani kwa uti? Iyai, inutu mudagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu, ndipo mai wanu adachotsedwa chifukwa cha upandu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Kalata wa chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayi anu ili kuti? Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole, ndinakugulitsani kwa ati? Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu; amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Kalata wa cilekaniro ca amako ali kuti amene ndinamsudzula naye? pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona cifukwa ca zoipa zanu munagulitsidwa, ndi cifukwa ca kulakwa kwanu amanu anacotsedwa.