Isaiah 50:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani mwa inu amaopa Chauta, ndi kumvera mau a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, wopanda chomuunikira, akhulupirire dzina la Chauta, ndipo adalire Mulungu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani mwa inu amaopa Yehova ndi kumvera mawu a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, popanda chomuwunikira, iye akhulupirire dzina la Yehova ndi kudalira Mulungu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wace? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wace.