Isaiah 50:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nonsenu amene mumasonkha moto ndi kuyatsa zikuni kuti muwononge anzanu, loŵani inuyo m'moto wanu womwewo, yendani pakati pa zikuni zimene mudayatsazo. Mudzakhala m'mazunzo, ndipo ndi Ineyo Chauta amene ndidzagwetsa mazunzowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'chuuno ndi nsakali, yendani inu m'chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha pa dzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu, lowani mʼmoto wanu womwewo. Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa. Ndipo ine Yehova ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'cuuno ndi nsakali, yendani inu m'cirangati ca moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ici mudzakhala naco ca pa dzanja langa; mudzagona pansi ndi cisoni.