Isaiah 50:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani panalibe anthu, pamene ndidabwera kudzaŵapulumutsa? Chifukwa chiyani panalibe wondiyankha, pamene ndidaitana? Kodi dzanja langa nloti nkulephera kuwombola? Kodi kapena ndilibe mphamvu zopulumutsira? Nditangodzudzula chabe, nyanja yaikulu itha kuuma, ndipo mitsinje itha kusanduka chipululu. Chifukwa chosoŵa madzi nsomba zam'menemo nkuyamba kununkha, ndiponso kufa ndi ludzu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, nizifa ndi ludzu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu? Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha? Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani? Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani? Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu, mitsinje ndinayisandutsa chipululu; nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi; ndipo zinafa ndi ludzu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa canji ndinafika osapeza munthu? ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja yaikuru, ndi kusandutsa mitsinje cipululu; nsomba zace zinunkha cifukwa mulibe madzi, nizifa ndi ludzu.