Isaiah 50:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso angandiimbe mlandu? Tipitire limodzi ku bwalo lamilandu. Wofuna kutsutsana nane ndani? Nabwere pafupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? Tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? Andiyandikire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso amene adzandiyimba mlandu? Abwere kuti tionane maso ndi maso! Mdani wanga ndi ndani? Abweretu kuti tilimbane!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? andiyandikire.