Isaiah 51:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti: “Tcherani khutu inu amene mufuna kupulumuka, inu amene mufuna kuti ndikuthandizeni. Taganizani za thanthwe kumene mudasemedwa, ku nkhuti ya miyala kumene adakukumbani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso ndiponso amene mumafunafuna Yehova: Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mverani Ine, inu amene mutsata cilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani ikuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.