Isaiah 51:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi sindinu amene mudaumitsa nyanja yaikulu ija, madzi ozama kwambiri? Kodi sindinu amene mudapanga njira pa madzi, kuti amene mudaŵapulumutsa aoloke pouma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu, madzi ozama kwambiri aja? Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama, kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; amene anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?