Isaiah 51:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta, Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo, ndi kuika maziko a dziko lapansi? Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse muziwopa ukali wa anthu okuzunzani, amene angofuna kukuwonongani? Ukali wa anthu okuzunzaniwo tsopano uli kuti?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu, amene anayala za mlengalenga ndi kuyika maziko a dziko lapansi. Inu nthawi zonse mumaopsezedwa chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani amene angofuna kukuwonongani. Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse cifukwa ca ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? uli kuti ukali wa wotsendereza?