Isaiah 51:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mavuto akugwera paŵiri: dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka, ndipo anthu ako apululuka ndi njala ndi nkhondo. Ndani angakumvere chifundo? Ndani angakutonthoze mtima?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? Bwinja ndi chipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mavuto awiriwa akugwera iwe. Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga. Ndani angakumvere chisoni? Ndani angakutonthoze?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? bwinja ndi cipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji?