Isaiah 51:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Taganizani za Abrahamu, bambo wanu ndi Sara amene adakubalani. Pamene ndinkamuitana Abrahamu, adaalibe mwana. Koma ndidamudalitsa, ndidampatsa ana, ndipo ndidachulukitsa zidzukulu zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
taganizani za Abrahamu, kholo lanu, ndi Sara, amene anakubalani. Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana, koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumcurukitsa.