Isaiah 51:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana ako akomoka, ali ngundangunda pa miseu yonse ngati mphoyo zokodwa mu ukonde. Kwaŵagwera kukwiya kwa Chauta ndi kudzudzula kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana ako amuna akomoka; agona pamtu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana ako akomoka; ali lambalamba pa msewu, ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde. Ukali wa Yehova ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana ako amuna akomoka; agona pamtu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako,