Isaiah 51:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikhocho ndidzachipereka kwa okuzunza, amene adaakuuza kuti, ‘Gona pansi, tikuyende pamsana.’ Msana wako adauyesa pansi popondapo, adauyesa mseu woti ayendepo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzachiika m'dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza, amene ankakuwuza kuti, ‘gona pansi tikuyende pa msana.’ Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo, ngati msewu woti ayendepo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzaciika m'dzanja la iwo amene abvutitsa iwe; amene anena ku moyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.