Isaiah 51:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi nkhwangwara yake ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzatonthozadi Ziyoni, ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse; Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni, malo ake owuma ngati munda wa Yehova. Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda ndi kundiyamika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ace onse abwinja; ndipo wasandutsa cipululu cace ngati Edene, ndi nkhwangwara yace ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.