Isaiah 51:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzabwera mofulumira kudzaombola anthu anga, nthaŵi yanga ya kuŵapulumutsa ili pafupi. Ine mwiniwakene ndidzalamulira mitundu ya anthu onse. Maiko akutali akundidikira kuti ndibwere, akundiyembekeza ndi chikhulupiriro kuti ndidzaŵapulumutse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga. Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga; ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse. Mayiko akutali akundiyembekezera. Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cilungamo canga ciripafupi, cipulumutso canga camuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.