Isaiah 51:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yang'anani mlengalenga, yang'anani dziko lapansi. Mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala, ndipo anthu ake onse adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, ndipo kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwezani maso anu mlengalenga, yangʼanani pansi pa dziko; mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko; pakuti kumwamba kudzacoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati copfunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa cimodzimodzi; koma cipulumutso canga cidzakhala ku nthawi lonse, ndi cilungamo canga sicidzacotsedwa.