Isaiah 51:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi, anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu; musaope kudzudzulidwa ndi anthu kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mverani Ine, inu amene mudziwa cilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope citonzo ca anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.