Isaiah 51:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu otereŵa adzatha ngati nsalu yodyewa ndi njenjete, adzatha ngati thonje lodyewa ndi mbozi. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala; mbozi idzawadya ngati thonje. Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya, chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti njenjete idzawadya ngati copfunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma cilungamo canga cidzakhala ku nthawi zonse, ndi cipulumutso canga ku mibadwo yonse.