Isaiah 52:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika pamaso pa anthu a mitundu yonse, ndipo anthu onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wabvula mkono wace woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona cipulumutso ca Mulungu wathu.