Isaiah 52:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika, kotero kuti siinkachitanso ngati ya munthu. Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu. Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israyeli, momwemo nkhope yace yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ace kupambana ana a anthu;