Isaiah 52:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzimodzinso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, Mafumu omwe adzasoŵa naye chonena, popeza kuti zinthu zosaŵauzapo chiyambire adzaziwona, ndipo zinthu zosamvapo nkale lonse, adzazimvetsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwa kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye. Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona, ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti cimene sicinauzidwa kwa iwo adzaciona, ndi cimene iwo sanamva adzazindikira.