Isaiah 52:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine Chauta ndikunena kuti, ‘Tsopano nditani poona kuti anthu anganu adakutengani ukapolo osaperekapo kanthu? Okulamulani akufuula monyodola, ndipo angokhalira kundinyoza kosalekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Ine Yehova ndikuti, “Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu, amene amawalamulira amawanyoza,” akutero Yehova. “Ndipo tsiku lonse, akungokhalira kuchita chipongwe dzina langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace kodi ndicitenji pano? ati Yehova; popeza anthu anga acotsedwa popanda kanthu? akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa licitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.