Isaiah 53:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa. Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa. Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wace ukapereka nsembe yoparamula, Iye adzaona mbeu yace, adzatanimphitsa masiku ace; ndipo comkondweretsa Yehova cidzakula m'manja mwace.