Isaiah 53:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye adzaona zotsatira mabvuto a moyo wace, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zace mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.