Isaiah 53:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu, adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza anapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe. Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri, ndipo anawapempherera anthu olakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndidzamgawira gawo ndi akuru; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wace kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula macimo a ambiri, napembedzera olakwa.