Isaiah 53:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye uja anthu adamnyoza ndipo adamkana. Anali munthu wamasautso, wozoloŵera zoŵaŵa. Anali ngati munthu amene anzake amaphimba kumaso akamuwona. Anthu adamnyoza, ndipo ife sitidamuyese kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu, munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa, ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona. Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza.