Isaiah 53:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuvesa wokhomedwa wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa.