Isaiah 53:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamgwira mwankhanza namuzenga mlandu, ndipo adapita naye kukamupha. Mwa anthu anzake ndani adalabadako zoti iye adachotsedwa m'dziko la anthu amoyo? Ndani adalabadako kuti iye uja adalangidwa chifukwa cha machimo a anthu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake, poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo? Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anacotsedwa ku cipsinjo ndi ciweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wace? pakuti walikhidwa kunja kuno; cifukwa ca kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.