Isaiah 53:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamkonzera manda ake pakati pa manda a achifwamba. Adamuika m'manda pakati pa anthu olemera, ngakhale iye sadachitepo chosalungama chilichonse ndipo sadanene bodza lililonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipa ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma, ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa, kapena kuyankhula za chinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika manda ace pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yace, ngakhale Iye sanacita ciwawa, ndipo m'kamwa mwace munalibe cinyengo.