Isaiah 54:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Fuula ndi chimwemwe iwe Yerusalemu amene wakhala ngati chumba chopanda ana, fuula mosangalala, iwe amene sudamvepo zoŵaŵa za kubala. Pakuti tsopano udzakhala ndi ana ochuluka kuposa mkazi amene sadasiyidweko ndi mwamuna wake,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imba, iwe wouma, amene sunabala; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Sangalala, iwe mayi wosabala, iwe amene sunabalepo mwana; imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yimba, iwe wouma, amene sunabala; yimba zolimba ndi kupfuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa acuruka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.