Isaiah 54:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzamanga nsanja zako ndi miyala yofiira. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yochezimira ngati moto. Ndidzamanganso linga lokuzungulira ndi miyala ya mtengo wapatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto, ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.