Isaiah 54:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni: Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse. Sudzakhalanso ndi mantha chifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'cilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutari ndi cipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutari ndi mantha, pakuti sadzafika cifupi ndi iwe.