Isaiah 54:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati wina autsa nkhondo, si ndine ndachititsa ai. Amene alimbana nawe adzalephera, poti udzaŵagonjetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; amene aliyense adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa chifukwa cha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina adzakuthirani nkhondo, si ndine amene ndachititsa; aliyense amene adzalimbana nanu adzagonja chifukwa cha iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; amene ali yense adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa cifukwa ca iwe.