Isaiah 54:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula, amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida. Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Taona, ndi Ine amene ndinalenga munthu wosula zitsulo amene amakoleza moto wamakala ndi kusula zida zoti azigwiritse ntchito. Ndipo ndine amene ndinalenga munthu wosakaza kuti awononge;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ndalenga wacipala amene abvukuta moto wamakala, ndi kuturutsamo cida ca nchito yace; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.