Isaiah 54:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzasendeza malire ake uku ndi uku. Zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina, zidzadzaza mizinda imene idasiyidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu cholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere; ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina ndipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu colowa cao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.