Isaiah 54:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaakufulatira pa mphindi yaing'ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa ndili wokwiya kwambiri. Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya, ndidzakuchitira chifundo,” akutero Yehova Mpulumutsi wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa cikhalire ndidzakucitira cifundo, ati Yehova Mombolo wako.