Isaiah 54:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kwa ine zimenezi zili monga m'mene zinaliri nthaŵi ya Nowa: monga momwe ndidaalumbirira nthaŵi imeneyo kuti sindidzaononganso dziko lapansi ndi chigumula, chonchonso tsopano ndikulumbiranso kuti sindidzakupseranso mtima, ndipo sindidzakudzudzulanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso pa dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa. Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi. Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima, sindidzakudzudzulaninso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso pa dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.