Isaiah 55:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.