Isaiah 55:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe ndipo adzakutsogolerani mwamtendere; mapiri ndi zitunda zidzakuyimbirani nyimbo, ndipo mitengo yonse yamʼthengo idzakuwombereni mʼmanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti inu mudzaturuka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzayimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.