Isaiah 55:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano mudzaitana mitundu imene simuidziŵa. Mitundu imene sikudziŵani idzabwera ndi liŵiro kuti ikhale nanu, chifukwa cha Ine Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, amene ndidakupatsani ulemerero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwa, ndi mtundu umene sunakudziwa udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa, ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu. Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu, Woyerayo wa Israeli, wakuvekani ulemerero.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwa, ndi mtundu umene sunakudziwa udzakuthamangira, cifukwa ca Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli; pakuti Iye wakukometsa.