Isaiah 55:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitari kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.