Isaiah 56:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri onse a Israele ndi akhungu, onsewo ndi opanda nzeru konse. Ali ngati agalu opanda mau, osatha kuuwa. Ntchito nkulota, kugona pansi, kukondetsa tulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu, onse ndi opanda nzeru; onse ndi agalu opanda mawu, samatha kuwuwa: amagona pansi nʼkumalota amakonda kugona tulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alonda ace ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agaru acete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.