Isaiah 56:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali ngati agalu a njala yaikulu, amene sakhuta konse. Abusa nawonso ndi opanda nzeru. Aliyense amachita monga m'mene afunira, ndipo amangofuna zokomera iye yekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m'dera lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu; sakhuta konse. Abusa nawonso samvetsa zinthu; onse amachita monga akufunira, aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde agaru ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira ku njira zao, yense kutsata phindu lace m'dera lace.