Isaiah 56:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zidakwa zimenezi zimati, ‘Tiyeni timwe vinyo, tiyeni timwe zakumwa zamphamvu mpaka kukhuta. Maŵa lidzakhala ngati leroli, mwina mwake nkudzaposa lero limene.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo! Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta! Mawa lidzakhala ngati leroli, kapena kuposa lero lino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta cakumwa caukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikuru loposa ndithu.